Yehova Amatithandiza

Testemunhas de Jeová (jw.org)

Compositor: Não Disponível

Ndinkachitadi mantha
Ndinali wosatetezeka
Ndinkatsutsidwa kwambiri
Koma ndalimba mtima
Iye wati ndim’dalire
Ndithu anditeteza
Amandikondadi
Wan’thandiza
Kulimba n’tafooka
Kulimba n’tatha nzeru
Kulimba m’mayesero
Kupirira ndithu
Kulimba m’mavuto
Kum’dalira nthawi zonse
Yehova ’mandithandiza
Wan’dziwitsa
Njira zake
Zomwe n’zolungama
An’thandiza
Kuti ndimvetse
N’kudziperekabe
Sulitu wekha
Ngakhale unachoka
Ali nawe
Akuthandiza
Kuti upirirebe ndithu
N’kukupatsa nzeru
Akuthandiza
Kulimba ukafo’ka
Kulimba zikavuta
Kulimba m’mayesero
Kupirira ndithu
Kulimba m’mavuto
Kum’dalira nthawi zonse
Yehova ’matithandiza​

M’zonse, m’zonse
Yehova ’matithandiza
Tadziwatu ndithu
Njira zake
Zomwe n’zolungama
Yehova ’matithandiza
Athandiza
Kuti timvetse
N’kudziperekabe
Ndinatha
Kulimba n’tafooka
Kulimba n’tatha nzeru
Kulimba m’mayesero
Kupirira ndithu
Kulimba m’mavuto
Kum’dalira nthawi zonse
Yehova ’matithandiza​
M’zonse, m’zonse
Yehova ’matithandiza​
M’zonse, m’zonse
Yehova ’matithandiza

©2003- 2024 lyrics.com.br · Aviso Legal · Política de Privacidade · Fale Conosco desenvolvido por Studio Sol Comunicação Digital